Jeremiah 11:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidakhala ngati mwanawankhosa amene akupita naye kokamupha. Sindidadziŵe kuti chidaloza pa ine chiwembu chimene ankakonzekera nkumanena kuti, “Tiyeni tiwudule mtengowu ukali moyo. Tiyeni timuphe munthu ameneyu, kuti asadzakumbukikenso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine ndinanga mwanawankhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwa kuti anandichitira ine chiwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zake, timdule iye pa dziko la amoyo, kuti dzina lake lisakumbukikenso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinali ngati mwana wankhosa wofatsa amene akupita naye kukamupha; sindinkadziwa kuti chiwembu chimene ankakonzekeracho chinkaloza ine. Iwo amati: “Tiyeni timuphe munthu ameneyu kuti dzina lake lisadzakumbukiridwenso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine ndinanga mwana wa nkhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwa kuti anandicitira ine ciwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zace, timdule iye pa dziko la amoyo, kuti dzina lace lisakumbukikenso.