Jeremiah 11:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta Wamphamvuzonse amene mumaweruza molungama, amene mumayesa mtima ndi maganizo, onetseni kuti mwaŵalipsira, pajatu ndidadzipereka m'manja mwanu!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma, Yehova wa makamu, amene aweruza molungama, amene ayesa impso ndi mtima, ndikuoneni Inu mulikuwabwezera chilango, pakuti kwa Inu ndawulula mlandu wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumaweruza molungama ndi kuyesa mitima ndi maganizo, lolani kuti ine ndione kuti mwawalipsira, pakuti mlandu wanga ndawupereka mʼmanja mwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma, Yehova wa makamu, amene aweruza molungama, pamene ayesa imso ndi mtima, ndikuoneni Inu mulikuwabwezera cilango, pakuti kwa Inu ndaulula mlandu wanga.