Jeremiah 11:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho ndidzachita zimene ndidalonjeza makolo anu molumbira, zakuti ndidzaŵapatsa dziko lamwanaalirenji, dziko limene mukukhalamoli.’ ” Tsono ine ndidayankha kuti, “Zikhale momwemo, Inu Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti ndikalimbikitse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu, ndiwapatse dziko moyenda mkaka ndi uchi, monga lero lomwe. Ndipo ndinayankha, ndi kuti, Amen, Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Ine ndidzakwaniritsa lumbiro lomwe ndinalumbira kwa makolo anu kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,’ dziko lomwe inu lero mukukhalamo.” Tsono Ine ndinayankha kuti, “Ameni, Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti ndikalimbikitse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu, ndiwapatse dziko mayenda mkaka ndi uci, monga lero lomwe. Ndipo ndinayankha, ndi kuti, Amen, Yehova.