Jeremiah 11:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Ulalike mau onseŵa ku mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu. Uŵauze kuti, ‘Imvani mau a chipangano ichi, ndipo muŵasunge.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau aonsewa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwachita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anandiwuza kuti, “Lengeza mawu onsewa mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu: ‘Mverani mawu a pangano ili ndi kuzitsatira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa ine, Lalikira mau onsewa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, kuti, Tamvani mau a pangano ili, ndi kuwacita.