Jeremiah 11:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ndi nthaŵi ndakhala ndikuŵachenjeza makolo anu kuyambira pamene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito mpaka lero lino. Ndakhala ndikuŵauza kuti, “Mverani mau anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndinatsimikizitsa kwa atate anu tsiku lomwe ndinawatulutsa iwo kudziko la Ejipito, mpaka lero lomwe, kuuka mamawa ndi kutsimikiza, kuti, Mverani mau anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyambira nthawi imene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto mpaka lero, ndakhala ndi kuwachenjeza kawirikawiri kuti, ‘Mverani Ine.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndinatsimikizitsa kwa atate anu tsiku lomwe ndinawaturutsa iwo ku dziko la Aigupto, mpaka lero lomwe, kuuka mamawa ndi kutsimikiza, kuti, Mverani mau anga.