Jeremiah 11:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma sadamvere, sadalabadeko. Aliyense adangoti nkhongo gwa, kutsata makhalidwe a mtima wake woipa. Ndidaŵalamula kuti asunge chipangano changa, koma iwo sadachisunge. Nchifukwa chake ndidaŵalanga monga m'mene ndidaanenera.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma sanamvere, sanatchere khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; chifukwa chake ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti achite, koma sanachite.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma sanamvere kapena kulabadirako. Aliyense anawumirira kuchita zoyipa za mʼmitima yawo. Ngakhale ndinawalamulira kuti asunge pangano langa koma iwo sanasunge. Choncho ndinawalanga monga ndinaneneramo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; cifukwa cace ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti acite, koma sanacita.