Jeremiah 12:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta nditati nditsutsane nanu, wokhoza ndinu ndithu. Komabe ndifuna kudandaulako kwa Inu za mlandu wanga. Chifukwa chiyani anthu oipa zinthu zimaŵayendera bwino? Chifukwa chiyani anthu osakhulupirika amakhala pabwino?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; chifukwa chanji ipindula njira ya oipa? Chifukwa chanji akhala bwino onyengetsa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova, Inu mumakhala wokhoza nthawi zonse ndikati nditsutsane nanu. Komabe ndikufuna kuyankhula nanu za mlandu wanga. Chifukwa chiyani anthu oyipa zinthu zimawayendera bwino? Chifukwa chiyani anthu achinyengo amakhala pabwino?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wolungama ndinu, Yehova, pamene nditsutsana nanu mlandu; pokhapo ndinenane nanu za maweruzo; cifukwa canji ipindula njira ya oipa? cifukwa canji akhala bwino onyengetsa?