Jeremiah 12:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu adafesa tirigu, koma adakolola minga. Adadzitopetsa pogwira ntchito, koma osapindula nkanthu komwe. Zokolola zao nzochititsa manyazi, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abzala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu anafesa tirigu koma anatuta minga; anadzitopetsa kugwira ntchito koma osapeza phindu lililonse. Choncho mudzachita manyazi ndi zokolola zanu chifukwa cha mkwiyo wa Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abzyala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, cifukwa ca mkwiyo woopsya wa Yehova.