Jeremiah 12:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Anthu oipa onse oyandikana ndi Aisraele, akulanda Aisraelowo dziko, choloŵa chimene ndidapatsa anthu angawo. Nchifukwa chake ndidzaŵachotsa m'dziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova ponenera anansi anga onse oipa, amene akhudza cholowa chimene ndalowetsamo anthu anga Israele; taonani, ndidzazula iwo m'dziko lao, ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu oyipa oyandikana ndi anthu anga Aisraeli, akuwalanda Aisraeliwo dziko, cholowa chimene ndinawapatsa. Nʼchifukwa chake ndidzawachotsa mʼdziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova ponenera anansi anga onse oipa, amene akhudza colowa cimene ndalowetsamo anthu anga Israyeli; taonani, ndidzazula iwo m'dziko lao, ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pao.