Jeremiah 12:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iwo akadzaphunzira bwino njira za mayendedwe a anthu anga, ndi kumalumbira m'dzina langa kuti, ‘Pali Chauta Wamoyo,’ monga momwe iwo adaphunzitsira anthu anga kumalumbira m'dzina la Baala, ndiye kuti iwowo ndidzaŵakhazikitsa pakati pa anthu anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira pali Baala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati iwo adzaphunzira bwino njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa, namanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ monga iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, Ine ndidzawakhazikitsa pakati pa anthu anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika