Jeremiah 12:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Inu Chauta ine mumandidziŵa. Mumandiyang'ana, ndipo mumayesa mtima wanga, nkuwona kuti ndimakukondani. Muŵakoke anthu oipa ngati nkhosa zokaphedwa. Muŵaike padera mpaka tsiku loti akaphedwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwatulutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Inu Yehova, ine mumandidziwa; mumandiona ndipo mumayesa zolingalira zanga. Akokeni anthu oyipawo ngati nkhosa zokaphedwa! Ayikeni padera mpaka tsiku loti akaphedwe!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwaturutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.