Jeremiah 12:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti? Ndipo udzu wake udzakhalabe wouma mpaka liti? Palibe mbalame kapena nyama zimene zatsala chifukwa anthu okhalamo ndi oipa kwambiri. Amati, “Mulungu sadzaona zimene zidzatiwonekere masiku athu otsiriza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti ndipo udzu mʼmunda uliwonse udzakhalabe ofota mpaka liti? Nyama ndi mbalame kulibiretu chifukwa anthu amene amakhalamo ndi oyipa. Iwo amati: “Yehova sangathe kuona ntchito zathu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? cifukwa ca zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona citsiriziro cathu.