Jeremiah 12:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga ndi anthu, nanga udzapikisana bwanji ndi akavalo? Ngati mtima wako ulefuka m'dziko lokoma, nanga udzatani m'nkhalango ya ku Yordani?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati wathamanga pamodzi ndi oyenda pansi, ndipo iwo anakulemetsa iwe, udzayesana nao akavalo bwanji? Ndipo ngakhale ukhazikika m'dziko lamtendere, udzachita chiyani m'kudzikuza kwa Yordani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga pamodzi ndi anthu nanga ungapikisane bwanji ndi akavalo? Ngati ukupunthwa ndi kugwa pa malo abwino, udzatha bwanji kuthamanga mʼnkhalango za ku Yorodani?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati wathamanga pamodzi ndi oyenda pansi, ndipo iwo anakulemetsa iwe, udzayesana nao akavalo bwanji? ndipo ngakhale ukhazikika m'dziko lamtendere, udzacita ciani m'kudzikuza kwa Yordano?