Jeremiah 12:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu anga osankhidwa asanduka ngati mikango yakuthengo, amandidzumira mwaukali. Nchifukwa chake ndimadana nawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Cholowa changa chandisandukira mkango wa m'nkhalango; anatsutsana nane ndi mau ake; chifukwa chake ndinamuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu amene ndinawasankha asanduka ngati mkango wa mʼnkhalango. Akundibangulira mwaukali; nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Colowa canga candisandukira mkango wa m'nkhalango; anatsutsana nane ndi mau ace; cifukwa cace ndinamuda.