Jeremiah 12:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu anga osankhidwa ali ngati mbalame yamaŵangamaŵanga imene akabaŵi aizinga kuchokera konsekonse. Kasonkhanitseni nyama zakuthengo, mubwere nazo ku phwando.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Cholowa changa chili kwa ine ngati mbalame yamawalamawala yolusa? Kodi mbalame zolusa zimzinga ndi kudana naye? Mukani, musonkhanitse zilombo za m'thengo, mudze nazo zidye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu anga amene ndinawasankha asanduka ngati mbalame yolusa yamawangamawanga imene akabawi ayizinga. Pitani, kasonkhanitseni nyama zakuthengo. Mubwere nazo kuti zidzadye mbalameyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Colowa canga ciri kwa ine ngati mbalame yamawala-mawala yolusa? kodi mbalame zolusa zimzinga ndi kudana naye? mukani, musonkhanitse zirombo za m'thengo, mudze nazo zidye.