Jeremiah 13:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu oipaŵa akana kumvera mau anga. Atsata milungu ina, namaitumikira nkumaipembedza. Iwowo adzakhala ngati mpango wopanda ntchitowu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu yina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.