Jeremiah 13:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga mpango umakanirira m'chiwuno mwa munthu, chonchonso ndidakonza kuti banja lonse la Israele ndi la Yuda lindikangamire kuti onse akhale anthu anga, kuti adzatamande dzina langa ndi kundilemekeza. Koma iwowo sadamvere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti monga mpango uthina m'chuuno cha munthu, chomwecho ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israele ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi chilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti monga mpango uthina m'cuuno ca munthu, comweco ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israyeli ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi cilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva.