Jeremiah 13:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ukaŵauze anthu mau amene Ine Chauta Mulungu wa Israele ndikunena, akuti: Mtsuko uliwonse wa vinyo adzaudzaza ndi vinyo. Iwowo adzakuyankha kuti, ‘Tikudziŵa bwino kuti mtsuko uliwonse wa vinyo adzaudzaza ndi vinyo.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake uzinena ndi iwo mau awa: Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo; ndipo adzati kwa iwe, Kodi sitidziwitsa bwino kuti matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Awuze anthuwo kuti, ‘Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Mtsuko uliwonse adzawudzaza ndi vinyo.’ Ndipo ngati iwo anena kwa iwe kuti, ‘Kodi ngati ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse udzadzazidwa ndi vinyo?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace uzinena ndi iwo mau awa: Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo; ndipo adzati kwa iwe, Kodi sitidziwitsa bwino kuti matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo?