Jeremiah 13:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha, atate ndi ana ao!” Akuterotu Chauta. “Sindidzaŵachitira chifundo kapena kuŵamvera chisoni, kapena kukhululuka mtima mpaka nditaŵaononga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzaphwanyanitsa wina ndi wina, atate ndi ana, ati Yehova; sindidzakhala ndi chisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi chifundo, chakuti ndisawaononge.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzaphwanyanitsa wina ndi wina, atate ndi ana, ati Yehova; sindidzakhala ndi cisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi cifundo, cakuti ndisawaononge.