Jeremiah 13:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mukapanda kumvera, mtima wanga udzalira m'seri chifukwa cha kunyada kwanu. M'maso mwanga mudzadzaza misozi yoŵaŵa chifukwa choti nkhosa za Chauta zatengedwa ukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri chifukwa cha kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, chifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati simumvera, ndidzalira kwambiri chifukwa cha kunyada kwanu. Mʼmaso mwanga mwadzaza ndi misozi yowawa chifukwa nkhosa za Yehova zatengedwa ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri cifukwa ca kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, cifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.