Jeremiah 13:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uza mfumu pamodzi ndi mai wake kuti, “Tsikani pa mipando yaufumu, poti zisoti zanu zokongola zaufumu zagwa pansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti, “Tsikani pa mipando yaufumuyo, pakuti zipewa zanu zaufumu zokongolazo zagwa pansi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nenani kwa mfumu ndi kwa amace wa mfumu, Dzicepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.