Jeremiah 13:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mizinda yanu ya ku Negebu aitsekera kunja, palibe wina woti nkuitsekula. Yuda yense watengedwa ukapolo, watengedwa yense ukapolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Midzi ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda wonse wachotsedwa m'ndende wonsewo, wachotsedwa m'nsinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa ndipo palibe wina woti nʼkuyitsekula. Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo, watengedwa yense ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Midzi ya ku Mwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda wonse wacotsedwa m'ndende wonsewo, wacotsedwa m'nsinga.