Jeremiah 13:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi mudzatani akadzakuikirani kuti azikulamulirani anthu amene munkaŵayesa abwenzi anu? Kodi simudzamva zoŵaŵa zonga za mkazi pa nthaŵi yochira?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzanena chiyani pamene adzaika abale ako akulu ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? Kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira anthu amene unkanena kuti ndi abale ako akukugonjetsa ndi kukulamulira? Kodi sudzamva zowawa ngati za mayi pa nthawi yake yochira?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzanena ciani pamene adzaika abale ako akuru ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala?