Jeremiah 13:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukamadzifunsa kuti, ‘Kodi zimenezi zatigwera bwanji?’ Nchifukwa cha machimo anu ambiri kuti zovala zanu zikwinzidwe, ndipo kuti akuchiteni zankhanza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine chifukwa ninji? Chifukwa cha choipa chako chachikulu nsalu zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zithende zako zaphwetekwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati udzadzifunsa kuti, “Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?” Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri kuti zovala zanu zingʼambike ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine cifukwa ninji? Cifukwa ca coipa cako cacikuru nsaru zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zithende zako zaphwetekwa.