Jeremiah 13:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patapita masiku ambiri Chauta adandiwuza kuti, “Nyamuka, pita ku Yufurate, ukatenge mpango wam'chiwuno uja umene ndidaakuuza kuti ukaubise kumeneko.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati mwa ine, Uka, pita ku Yufurate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patapita masiku ambiri Yehova anandiwuzanso kuti, “Pitanso ku Yufurate ndipo ukatenge lamba amene ndinakuwuza kuti ukamubise kumeneko.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati kwa ine, Uka, pita ku Firate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.