Jeremiah 14:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena za anthu ameneŵa kuti, “Amakonda kuyendayenda kumene afuna, ndipo sangathe kudziletsa. Nchifukwa chake Ine Chauta sindingakondwere nawo, ndipo tsopano ndidzakumbukira kuipa kwao, ndidzaŵalanga chifukwa cha machimo ao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova kwa anthu awa, Chomwecho akonda kusocherera; sanakanize mapazi ao; chifukwa chake Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira choipa chao, nadzalanga zochimwa zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimene Yehova akunena za anthuwa ndi izi: “Iwo amakonda kuyendayenda kwambiri; samatha kudziretsa. Nʼchifukwa chake Ine Yehova sindingawalandire, ndipo tsopano ndidzakumbukira zoyipa zawo ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova kwa anthu awa, Comwecoakonda kusocerera; sanakaniza mapazi ao; cifukwa cace. Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira coipa cao, nadzalanga zocimwa zao.