Jeremiah 14:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwao. Ndipo ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Koma ndidzaŵaononga ndi nkhondo, njala ndi mliri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi chaola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwawo; ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Mʼmalo mwake, ndidzawapha ndi lupanga, njala ndi mliri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene asala cakudya, sindidzamva kupfuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi cirala, ndi caola.