Jeremiah 14:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ine ndidati, “Ha, Inu Chauta, aneneri ao amauza anthu kuti sadzafa ndi nkhondo, ndipo simudzagwa njala m'dziko mwathu, koma mudzakhala mtendere wokhawokha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! Taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi chilala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova, aneneri amawawuza anthuwo kuti, sadzaphedwa ndi lupanga kapena kuvutika ndi njala. Koma kuti Inu mudzawapatsa mtendere wokhawokha pamalo pano.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi cirala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno.