Jeremiah 14:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti aneneri ameneŵa akulosa m'dzina langa pamene sindidaŵatume. Amakuuzani kuti simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala m'dziko lino. Koma aneneriwo ndiwo amene adzaphedwe pa nkhondo kapena kufa ndi njala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Yehova za aneneri onenera m'dzina langa, ndipo sindinawatuma, koma ati, Lupanga ndi chilala sizidzakhala m'dziko muno; ndi lupanga ndi chilala aneneriwo adzathedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti aneneri amenewa akulosera mʼdzina langa pamene Ine sindinawatume. Iwo amati simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala mʼdziko muno. Koma tsono ndi iwowo, aneneriwa amene adzafe pa nkhondo kapena ndi njala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Yehova za aneneri onenera m'dzina langa, ndipo sindinawatuma, koma ati, Lupanga ndi cirala sizidzakhala m'dziko muno; ndi lupanga ndi cirala aneneriwo adzathedwa.