Jeremiah 14:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene adaŵalosera adzaponyedwa m'miseu ya mu Yerusalemu, atafa pa nkhondo kapena ndi njala. Iwowo, akazi ao, ana ao aamuna ndi ana ao aakazi, onse adzafa, ndipo sipadzaoneka oika maliro ao. Ndithu ndidzaŵalanga poŵagwetsa m'mavuto oŵayenerera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu chifukwa cha chilala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna ndi aakazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anthu amene anawaloserawo adzaponyedwa mʼmisewu ya mu Yerusalemu atafa ndi njala ndi lupanga. Sipadzapezeka wowayika mʼmanda popeza iwowo, akazi awo, ana awo aamuna, onse adzakhala atafa. Ine ndidzawagwetsera chilango chowayenera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu amene adzanenera kwa inu adzaponyedwa kunja m'miseu ya Yerusalemu cifukwa ca cirala ndi lupanga; ndipo adzasowa akuwaika, ndi akazi ao, ndi ana ao amuna ndi akazi; ndipo ndidzatsanulira pa iwo zoipa zao.