Jeremiah 14:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikamayenda ku thengo, ndikuwona anthu ophedwa pa nkhondo. Ndikaloŵa mu mzinda, ndikuwona anthu ofa ndi njala. Aneneri ndi ansembe akupitirizabe ntchito zao m'dzikomo, koma osadziŵa zimene akuchita.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m'mudzi, taonani odwala ndi njala! Pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikapita kuthengo, ndikuona amene aphedwa ndi lupanga; ndikapita mu mzinda, ndikuona amene asakazidwa ndi njala. Ngakhale aneneri pamodzi ndi ansembe onse atengedwa.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndikaturukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! ndikalowa m'mudzi, taonani odwala ndi njala pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.