Jeremiah 14:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi anthu a ku Yuda mwaŵatayiratu? Kodi anthu a mu Ziyoni akuipirani m'maso? Chifukwa chiyani mwatikantha kotero kuti sitingathenso kukhala bwino? Tinkayembekeza mtendere, koma sitidaupeze. Tinkayembekeza kuchira, koma tidangoopsedwa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi mwakanadi Yuda? Kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? Bwanji mwatipanda ife, ndipo tilibe kuchira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakuchira, ndipo taonani mantha!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi anthu a ku Yuda mwawakana kwathunthu? Kodi mtima wanu wanyansidwa nawo anthu a ku Ziyoni? Chifukwa chiyani mwatikantha chotere kuti sitingathenso kuchira? Ife tinayembekezera mtendere koma palibe chabwino chomwe chabwera, tinayembekezera kuchira koma panali kuopsezedwa kokhakokha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi mwakanadi Yuda? kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? bwanji mwatipanda ife, ndipo tiribe kucira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakucira, ndipo taonani mantha!