Jeremiah 14:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musatikane, kuti dzina lanu linganyozeke. Musanyoze mpando wanu wachifumu ndi waulemerero. Mukumbukire chipangano chanu ndi ife, ndipo musachiphwanye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musatinyoze ife, chifukwa cha dzina lanu; musanyazitse mpando wachifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musatikane kuopa kuti dzina lanu linganyozedwe; musanyoze mpando wanu waufumu waulemerero. Kumbukirani pangano lanu ndi ife ndipo musachiphwanye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musatinyoze ife, cifukwa ca dzina lanu; musanyazitse mpando wacifumu wa ulemerero wanu; mukumbukire musasiye pangano lanu lopangana ndi ife.