Jeremiah 14:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakati pa milungu yonama ya anthu a mitundu ina, kodi alipo mulungu wina amene angathe kupereka mvula? Kodi mlengalenga umapereka mvula pawokha? Kodi Inu Chauta, suja ndinu nokha amene mumachita zimenezi? Nchifukwa chake timakhulupirira Inu, popeza kuti ndinu amene mumachita zinthu zonsezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa zachabe za mitundu ya anthu zilipo kodi, zimene zingathe kuvumbitsa mvula? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? Ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa milungu yachabechabe ya anthu a mitundu ina, kodi pali mulungu amene angagwetse mvula? Ife chikhulupiriro chathu chili pa Inu, popeza Inu nokha ndinu Yehova Mulungu wathu amene mukhoza kuchita zimenezi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa zacabe za mitundu ya anthu ziripo kodi, zimene zingathe kubvumbitsa mvula? Kodi si ndinu, Yehova, Mulungu wathu? ndipo tidzakudikirani Inu; pakuti munalenga zonse zimenezi.