Jeremiah 14:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri ao otchuka akutuma antchito ao kuti akatunge madzi. Apita ku zitsime, koma osapezako madzi, ndiye akubwerera ndi mitsuko yopanda kanthu. Achita manyazi ndipo atha nzeru, adziphimba kumaso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akulu ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, afunda mitu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu awo wolemekezeka akutuma antchito awo kuti akatunge madzi. Apita ku zitsime osapezako madzi. Choncho amabwerera ndi mitsuko yopanda madzi. Amanyazi ndi othedwa nzeru adziphimba kumaso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akuru ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, apfunda mitu yao.