Jeremiah 14:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu akuti, “Inu Chauta, ngakhale machimo athu akutipalamulitsa, komabe muchitepo kanthu kuti dzina lanu lisanyozeke. Kusakhulupirika kwathu nkwakukuludi. Takuchimwirani zedi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, chitani Inu chifukwa cha dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zachuluka; takuchimwirani Inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu akuti, “Ngakhale machimo athu akutitsutsa, koma Inu Yehova chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu. Pakuti kusakhulupirika kwathu nʼkwakukulu; ife takuchimwirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, citani Inu cifukwa ca dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zacuruka; takucimwirani Inu.