Jeremiah 14:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, amene muli chikhulupiriro cha Aisraele, ndiponso Mpulumutsi wao pa nthaŵi ya mavuto, mukukhaliranji ngati mlendo m'dziko lino, ngati wapaulendo wogona usiku umodzi?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu, chiyembekezo cha Israele, Mpulumutsi wake nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova amene Aisraeli amakukhulupirirani ndi amene mumawapulumutsa pa nthawi ya masautso, chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdziko muno? Chifukwa chiyani muli ngati wapaulendo amene akungogona tsiku limodzi?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu, ciyembekezo ca Israyeli, mpulumutsi wace nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?