Jeremiah 14:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wothedwa nzeru? Mukukhaliranji ngati wankhondo amene sangathenso kupulumutsa anthu? Komabe Inu Chauta, muli pakati pathu, ife amene timadziŵika ndi dzina lanu, choncho musatisiye tokha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? Koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, titchedwa ndi dzina lanu; musatisiye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani muli ngati munthu amene wadzidzimutsidwa, kapena ngati wankhondo amene alibe mphamvu yopulumutsa? Komabe Inu Yehova, muli pakati pathu, ndipo tikudziwika ndi dzina lanu; musatitaye ife!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, tichedwa ndi dzina lanu; musatisiye.