Jeremiah 15:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Chauta adandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga akupempherera anthu ameneŵa, sindikadaŵamvera chisoni. Achotseni, ndisaŵaonenso, apite basi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samueli akanayima pamaso panga kupempherera anthu awa, Ine sindikanawachitira chisoni. Achotseni ndipo ndisawaonenso! Aleke apite!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samueli akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwacotse iwo pamaso panga, aturuke.