Jeremiah 15:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mai wanga, tsoka kwa ine kuti mudandibala ine munthu wokangana ndi wotsutsana ndi anthu pa dziko lonse. Sindidakongole kanthu kwa munthu kapena kukongoza munthu kanthu. Komabe anthu onse akunditukwana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kalanga ine, amayi pakuti munandibereka ine, munthu amene ndikutsutsana ndi kulimbana ndi anthu pa dziko lonse! Ine sindinakongoze kapena kukongola kanthu, komatu aliyense akunditemberera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletsa paphindu; koma iwo onse anditemberera.