Jeremiah 15:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nditamva mau anu, ndidaŵalandira bwino, mauwo adandipatsa chimwemwe ndi chisangalalo. Paja Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndimadziŵika ndi dzina lanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino. Mawu anu anandipatsa chimwemwe ndipo mtima wanga unasangalala. Paja ine, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndimadziwika ndi dzina lanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine cikondwero ndi cisangalalo ca mtima wanga; pakuti ndachedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.