Jeremiah 15:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga chifukwa chiyani mavuto anga sakutha? Chilonda changa nchosatha, sichikupola. Monga nkuti mwandinyenga ngati chitsime chouma kapena ngati mtsinje wopanda madzi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kupweteka kwanga kuli chipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? Kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nanga nʼchifukwa chiyani mavuto anga sakutha? Bwanji chilonda changa sichikupola? Kodi inu mudzakhala ngati mtsinje wowuma nthawi yachilimwe, kapena ngati kasupe wopanda madzi?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kupweteka kwanga kuti cipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?