Jeremiah 15:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adayankha kuti, “Ukabwerera kwa Ine, ndidzakulandiranso, ndipo udzanditumikiranso. Ukamalankhula zenizeni, osati zachabe, udzakhala wondilankhulira. Anthu ameneŵa ayenera kudzabweranso kwa iwe, koma iwe usabwerere kwa iwowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Yehova, Ukabwerera pamenepo ndidzakubwezanso, kuti uime pamaso panga; ndipo ukasiyanitsa cha mtengo wake ndi chonyansa, udzakhala ngati m'kamwa mwanga; ndipo adzabwerera kwa iwe, koma sudzabwerera kwa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova anandiyankha kuti, “Ukabwerera kwa Ine, ndidzakulandiranso ndipo udzakhalanso mtumiki wanga. Ngati udzayankhula mawu oyenera osati achabechabe, udzakhalanso mneneri wanga. Anthu adzabwera kwa iwe ndipo sipadzafunika kuti iwe upite kwa iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Yehova, Ukabwerera pamenepo ndidzakubwezanso, kuti uime pamaso panga; ndipo ukasiyanitsa ca mtengo wace ndi conyansa, udzakhala ngati m'kamwa mwanga; ndipo adzabwerera kwa iwe, koma sudzabwerera kwa iwo.