Jeremiah 15:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akakufunsa kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ Uŵauze kuti Ine ndati, “ ‘Oyenera mliri adzafa ndi mliri, oyenera lupanga adzafa ndi lupanga, oyenera njala adzafa ndi njala, oyenera ukapolo, adzapita ku ukapolo.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titulukire kuti? Pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati akufunsa iwe kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ uwawuze kuti, ‘Yehova akuti, “ ‘Oyenera kufa adzafa; oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga; oyenera kufa ndi njala adzafa ndi njala; oyenera kupita ku ukapolo adzapita ku ukapolo.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titurukire kuti? pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga.