Jeremiah 15:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakusandutsa wolimba ngati linga lamkuŵa kwa anthuwo. Iwo adzalimbana nawe, koma sadzakupambana, pakuti Ine ndili nawe, ndidzakulanditsa ndi kukupulumutsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipo adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakusandutsa ngati khoma lolimba ngati mkuwa kwa anthu awa. Adzalimbana nawe koma sadzakugonjetsa, pakuti Ine ndili nawe kukulanditsa ndi kukupulumutsa,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipe adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndiri ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova.