Jeremiah 15:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzaŵagwetsera zinthu zinai izi zoŵaononga: lupanga loŵapha, agalu oŵaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zilombo zoti ziŵaphe ndi kuŵadya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agalu akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zilombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndidzawatumizira mitundu inayi ya zinthu zowononga,” akutero Yehova, “lupanga lowapha, agalu owaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zirombo zoti ziwadye ndi kuwawononga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agaru akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zirombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.