Jeremiah 15:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaŵabalalitsira uku ndi uku, monga momwe amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero. Ndidaŵaliritsa anthu anga ndi kuŵaononga, chifukwa sadafune kusiya makhalidwe ao oipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndawapeta ndi chopetera m'zipata za dziko; ndachotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzakubalalitsani kukuchotsani mʼmizinda ya mʼdzikomo monga mmene amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero. Anthu anga ndinawaliritsa ndi kuwawononga chifukwa sanasinthe makhalidwe awo oyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndawakupa ndi mkupo m'zipata za dziko; ndacotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao.