Jeremiah 15:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akazi amasiye ndidaŵachulukitsa, kupambana mchenga wakunyanja. Amai ndidaŵaonongera ana ao akali anyamata abiriŵiri. Mwadzidzidzi ndidaŵagwetsera chisoni ndi nkhaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinachulukitsa amayi awo amasiye kupambana mchenga wa kunyanja. Amayiwo ndinawawonongera ana awo aamuna dzuwa lili pamutu. Mwadzidzidzi ndinawagwetsera kuwawa mtima ndi mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amasiye ao andicurukira Ine kopambana mcenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.