Jeremiah 15:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mai wa ana asanu ndi aŵiri wakomoka, akupuma mwabefu. Mdima wamgwera kukadali masana. Adamchititsa manyazi ndipo wataya mtima. Otsala onse ndidzaŵapereka kwa adani kuti aŵaphe ndi lupanga,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lake lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayi wa ana asanu ndi awiri wakomoka ndipo akupuma wefuwefu. Dzuwa lake lalowa ukanali usana; anamuchititsa manyazi ndipo wathedwa nzeru. Otsala ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo kuti awaphe ndi lupanga,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lace lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova.