Jeremiah 16:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono ukadzaŵauza anthuwo mau ameneŵa, makamaka adzakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Chauta wanena kuti tsoka lotere lidzatigwera ifeyo? Kodi tidalakwanji? Kodi Inu Chauta, Mulungu wathu, takuchimwirani chiyani?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala, pamene udzaonetsa anthu awa mau awa onse, ndipo iwo adzati kwa iwe, Chifukwa chake nchiyani kuti Yehova watinenera ife choipa chachikulu ichi? Mphulupulu yathu ndi yanji? Tchimo lathu lanji limene tachimwira Yehova Mulungu wathu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ukawawuza anthu awa zinthu zonsezi akakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wanena kuti tsoka lalikulu lotere lidzatigwere? Kodi talakwa chiyani? Kodi tamuchimwira tchimo lotani Yehova Mulungu wathu?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala, pamene udzaonetsa anthu awa mau awa onse, ndipo iwo adzati kwa iwe, Cifukwa cace nciani kuti Yehova watinenera ife coipa cacikuru ici? mphulupulu yathu ndi yanji? cimo lathu lanji limene tacimwira Yehova Mulungu wathu?